ZIKHULUPIRIRO ZA MPINGO WATHU (Articles of Faith)

ZIKHULUPIRIRO ZA MPINGO WATHU
(ARTICLES OF FAITH)

Mulungu M'modzi Mwa Atatu

(The Truine God)

Timakhulupirira mwa Mulungu m'modzi amene ali wamuyaya ndi opanda malire. Iye ndiye Mulengi ndi olamulira kumwamba ndi dziko lapansi; Iye ndiye wochilikiza zinthu zones; Mulungu ndi woyera m’chikhalidwe chake chonse, chikondi chake ndi choyera ndi kuwala kwake ndi koyera, Mulungu ndi m'modzi amene anadziwonetsera mwa Atate, Mwana, ndi Mzimu Woyera.

[Genesis 1; Levitiko 19:2; Deutoronomo 6:4-5; Yesaya 5:16; 6:1-17; 40:18-31; Mateyu 3:16-17; 28:19-20; Yohane 14:6-27; 1 Akorinto 8:6; 2 Akorinto 13:14; Agalatia 4:4-6; Aefeso 2:13-18; 1 Yohane 1:5; 4:8]

Yesu Khristu (Jesus Christ)

Timakhulupirira mwa Yesu Khristu, yemwe ali wachiwiri mwa Utatu Woyera; amene wakhala ali mu umodzi ndi Atate; Iye akhala m’thupi kupyolera mwa Mzimu Woyera nabadwa mwa Maria namwaliyo, Yesu si munthu amene anasandulika kukhala Mulungu, kapena kuti Iye ndi Mulungu amene anangofuna kudziwonetsera ngati munthu. M'malo mwake Iye ndi Mulungu ndithu komanso ndi munthu ndithu: Mwa Iye munali Umulungu ndi umunthu umene unalumikizana kukhala m'modzi Mulungu.

Timakhulupirira kuti Yesu Khristu anafera machimo anthu ndipo anauka kwa akufa ndi thupi lake langwiro, Iye anakwera kumwamba kumene akutipembedzera.

[Mateyu 1:20-25; 16:15-16; Luka 1:26-35; Yohane 1:1-18; Machitidwe 2:22-36; Aroma 8:3, 32-34; Agalatia 4:4-5; Afilipi 2:5-11; Akolose 1:12-22; 1 Timoteo 6:14-16; Ahebri 1:1-5; 7:22-28; 9:24-28; 1 Yohane 1:1-3; 4:2-3, 15]

Mzimu Woyera (The Holy Spirit)

Timakhulupirira mwa Mzimu Woyera, yemwe ali wachitatu mu utatu wa Mulungu, Yemwe amagwira ntchito nthawi zonse mu mpingo wa Khristu, Iye amazindikilitsa dziko lapansi za tchimo, ndikupeleka moyo watsopano kwa iwo akulapa ndi kukhulupilira, Iye amayeretsa okhulupilira ndi kuwatsogolera iwo ku choonadi chonse chimene chili mwa Yesu.

[Yohane 7:39; 14:15-18, 26; 16:7-15; Machitidwe 2:33; 15:8-9; Aroma 8:1-27; Agalatia 3:1-14; 4:6; Aefeso 3:14-21; 1 Atesalonika 4:7-8; 2 Atesalonika 2:13; 1 Petro 1:2; 1 Yohane 3:24; 4:13]

Buku Lopatulika

(The Holy Scripture)

Timakhulupilira kuti Buku Lopatulika ndilouzilidwa kwathunthu ndi Mzimu Woyera, Timakhulupiriranso kuti mabuku 66 a m’Chipangano Chakale ndi Chatsopano, amatiwonetsera zonse zimene tikuyenera kuzidziwa zokhudzana ndi chipulumutso chathu, Zikhulupiliro zanthu zonse zikuyenera kutsamira pa Buku Lopatulika, kotero chimene sichipezeka m’Buku Lopatulika tisachitenge monga chikhulupiriro cha mpingo wanthu.

[Luka 24:44-47; Yohane 10:35; 1 Akorinto 15:3-4; 2 Timoteo 3:15-17; 1 Petro 1:10-12; 2 Petro 1:20-21]

Tchimo

(Sin)

Timakhulupirira kuti tchimo linadza m’dziko lapansi chifukwa cha kusamvera kwa makolo athu oyamba, ndipo imfa inadza chifukwa cha tchimo. Timakhulupirira kuti tchimo liri m'mitundu iwiri: tchimo lobadwa nalo ndi tchimo limene munthu amachita mwakusakha kwake.

Timakhulupirira kuti chifukwa cha tchimo lobadwa nalo, ndilo chivundi cha chikhalidwe chomwe chimapezeka mwa mbewu yonse ya Adamu pa chifukwa ichi aliyense wasochera kutali ndi chikhalidwe cha m’ngwiro chomwe makolo athu oyamba adali nacho panthawi imene iwo adalengedwa, Mulungu amaipidwa nacho chivundichi ndipo chilibe moyo wa uzimu, nthawi zonse chimachita uchimo, ndipo chasamira pa uchimo kosalekeza.  Timakhulupilira kuti chikhalidwe cha uchimu chimakhalabe mu mtima mwa m'khristu kufikira chikhalidwe cha uchimochi chitayeretsedwa kupyolera mu ubatizo wa Mzimu Woyera.

Timakhulupirira kuti tchimo lobadwa nalo ndilosiyana ndi tchimo limene munthu amachita mwakusakha kwake. Ichi ndichikhumokhumbo cha mkati mwathu chimene chimatipangitsa ife kuchita uchimo, anthu saweluzidwa chifukwa cha tchimo lobadwa nalo kufikira atanyozera kapena kukana dongosolo la Mulungu lothetsera tchimoli.

Timakhulupirira kuti tchimo lochita mwakusakha ndiko kuphwanya mwadala malamulo odziwika a Mulungu, munthu yekhayo amene ali nako kudzindikira kwa ntchito zake alinako kuthekera kochimwa mwadala. Machimo sali chimodzimodzi ndi zophophonya, zolephera, zolakwitsa, zofooka ndi zinthu zina zakudza mosayembekezera, zimene ziri zotsatira za chikhalidwe chathu cholephera ngati anthu. Komabe, malingaliro ndi machitachita amene ali osiyana ndi zofuna za Mzimu wa Khristu ndi machimo. Awa timawatcha machimo a mzimu. Tchimo lochita mwakusakha ndiko kuphwanya lamulo la chikondi ndi kusakhulupilira mwa Yesu Khristu.

[Tchimo Lobadwa Nalo: Genesis 3; 6:5; Yobu 15:14; Salimo 51:5; Yeremia 17:9-10; Marko 7:21-23; Aroma 1:18-25; 5:12-14; 7:1- 8:9; 1 Akorinto 3:1-4; Agalatia 5:16-25; 1 Yohane 1:7-8]

[Tchimo Lochita Mwakusakha: Mateyu 22:36-40 (pamodzi ndi 1 Yohane 3:4); Yohane 8:34-36; 16:8-9; Aroma 3:23; 6:15-23; 8:18-24; 14:23; 1 Yohane 1:9 – 2:4; 3:7-10]

Chiombolo

(Atonement)

Timakhulupirira kuti Yesu Khristu, anasautsidwa, ndi kukhetsa mwazi wake, ndikufa pa mtanda, kulipira ngongole ya machimo athu onse, ichi chimatchedwa chiombolo ndipo uku ndiko kukhazikitsika kokhako kwa chipulumutso chathu. Chiombolochi ndi cha chisomo ndipo chokwanira kupulumutsa osazindira ndi ana osaziwa kusankha pakati pa chabwino ndi choipa, komanso ndichokwainira kupulumutsa onse amene afika pamsinkhu wosankha pakati pa chabwino ndi choipa pokhapokha ngati iwo atalapa ndi kukhulupilira.

[Yesaya 53:5-6, Marko 10:45; Luka 24:46-48; Yohane 1:29; 3:14-17; Machitidwe 4:10-12; Aroma 3:21-26; 4:17-25; 5:6-21; 1 Akorinto 6:20; 2 Akorinto 5:14-21; Agalatia 1:3-4; 3:13-14; Akolose 1:19-23; 1 Timoteo 2:3-6; Tito 2:11-14; Ahebri 2:9; 9:11-14; 13:12; 1 Petro 1:18-21; 2:19-25; 1 Yohane 2:1-2]

Kupulumutsidwa mwa Chisomo

(Prevenient Grace)

Timakhulupirira kuti munthu aliyense analengedwa m'chifanizo chake cha Mulungu ichi chimatanthauza kuti anthu ali ndi kuthekera kosakha pakati pa chabwino ndi choipa, uwu ndi udindo umene tiri nawo pa zimene timachita; chifukwa cha kuchimwa kwa Adamu anthu onse amabadwa ndi chikhalidwe cha uchimo ndipo sangathe pa iwo okha kutembenukira kwa Mulungu kapena kuchita ntchito zabwino zimene zingathe kuwapulumutsa. Komabe timakhulupilira kuti chisomo cha Mulungu kupyolera mwa Yesu Khristu ndi chawulele kwa anthu onse, chisomo ichi chimapangitsa kuthekera kwa wina aliyense kusankha kusiya tchimo ndikusata chilungamo, kukhulupilira pa Yesu kuti ayeretsedwa kumachimo, ndikukhala moyo okondweretsa ndi ovomerezeka ndi Mulungu.

Timakhulupilira kuti ndi zotheka kwa iwo amene apulumutsidwa ndi kuyeretsedwa kubwereranso ku uchimo ndi kukana chikhulupiriro. Pokhapokha atalapa machimo awo, adzakhala opanda chiyembekezo ndi kutaika moyo wawo onse.

[Chifanizo Cha Mulungu ndi Udindo pa chikhalidwe: Genesisi 1:26-27; 2:16-17; Deutoronomo 28:1-2; 30:19; Yoswa 24:15; Salimo 8:3-5; Yesaya 1:8-10; Yeremia 31:29-30; Ezekieli 18:1-4; Mika 6:8; Aroma 1:19-20; 2:1-16; 14:7-12; Agalatia 6:7-8]

[Kulephera kwa chibadwidwe: Yobu 14:4; 15:14; Salimo 14:1-4; 51:5; Yohane 3:6a; Aroma 3:10-12; 5:12-14, 20a; 7:14-25]

[Chisomo cha ulere ndi ntchito za chikhulupiriro : Ezekieli 18:25-26; Yohane 1:12-13; 3:6b; Machitidwe 5:31; Aroma 5:6-8; 18; 6:15-16, 23; 10:6-8; 11:22; 1 Akorinto 2:9-14; 10:1-12; 2 Akorinto 5:18-19; Agalatia 5:6; Aefeso 2:8-10; Afilipi 2:12-13; Akolose 1:21-23; 2 Timoteo 4:10a; Tito 2:11-14; Ahebri 2:1-3; 3:12-15; 6:4-6; 10:26-31; Yakobo 2:18-22; 2 Petro 1:10-11; 2:20-22]

Kulapa

(Repentance)

Timakhulupirira kuti kulapa, kumene kuli kusinthika kwathunthu kwa moyo wa uzimu wa munthu wokhuzana ndi uchimo, kumene kumabwera chifukwa cha kutsutsika kwa chikumbu mtima  ndi kudzisankhira kuchoka ku uchimo, ndikofunika kwa aliyense amene anamuchimwira Mulungu. Mzimu wa Mulungu amapereka mwa chisomo kwa aliyense  amene akufuna kulapa mtima wakulapa ndi chiyembekezo cha chifundo, kuti iye akakhulupirire ndi kulandira chikhululukiro ndi moyo wa uzimu.

[2 Mbiri 7:14; Masalimo 32:5-6; 51:1-17; Yesaya 55:6-7; Yeremia 3:12-14; Ezekiel 18:30-32; 33; 14-16; Marko 1:14-15; Luka 3:1-14 13:1-5; 18:9-14; Machitdwe 2:38; 3:19; 5:31; 17:30-31; 26:16-18; Aroma 2:4; 2 Akorinto 7:8-11; 1 Atesalonika 1:9; 2 Petro 3:9]

Chilungamitso, Kubadwanso Kwatsopano, Ndi Kukhalanso Mwana Wa Mulungu

(Justification, Regeneration, and Adoption)

Timakhulupirira kuti onse amene amakhulupira Yesu Khristu ndi kumulandira Iye kukhala Mbuye ndi Mpulumutsi, ndi olungamitsidwa. Izi zikutathauza kuti Mulungu mwaulele amakhululukira zosalungama zawo ndi kuwamasula iwo kuzolakwa zawo. Amawalandira iwo ngati olungama.

Timakhulupirira kuti Mulungu amayeretsa mwa ulele onse akulapa ndi kulandira Yesu kukhala Mbuye ndi Mpulumutsi. Amawapatsa iwo moyo watsopano wa uzimu ndi chikhalidwe cha tsopano. Ichi chimatchedwa kubadwanso mwatsopano. Moyo watsopano umenewu ndi wachikhulupiriro, chikondi, ndi kumvera Mulungu.

Timakhulupirira kuti amene alungamitsa ndi kuyeretsa okhulupirira atsopano, amawalandira iwo m'banja la Mulungu.

Timakhulupirira kuti Chilungamitso, Kubadwa Mwatsopano, ndi Kukhalanso Mwana wa Mulungu zonsezi zimachitika nthawi imodzi kwa munthu amene akufuna Mulungu, ndipo izi zimalandiridwa ngati tili ndi chikhulupiriro, potsatiridwa ndi kulapa; Timakhulupiriranso kuti Mzimu Woyera amachitira umboni pa ntchito za chisomo zimenezi

[Luka 18:14; Yohane 1:12-13;3:3-8; 5:24; Machitidwe 13:39; Aroma 1:17; 3:21-26, 28; 4:5-9; 17-25; 5:1, 16-19; 6:4; 7:6; 8:1, 15-17; 1 Akorinto 1:30; 6 :11; 2 Akrinto 5:17-21; Agalatia 2:16-21; 3:1-14, 26; 4:4-7; Aefeso 1:6-7; 2:1, 4-5; Afilipi 3:3-9; Akolose 2:13; Tito 3:4-7; 1 Petro 1:23; 1 Yohane 1:9; 3:1-2, 9; 4:7; 5:1, 9-13, 18]

Chiyelo cha Chikhristu ndi Chiyeretso Chathunthu

(Christian Holiness & Entire Sanctification)

Timakhulupirira kuti chiyeretso ndi ntchito ya Mulungu imene imasunduliza okhulupirira kuti afanane ndi Yesu. Chisomo cha Mulungu ichi chimakwaniritsidwa ndi Mzimu Woyera pakupita kwa nthawi, chimayamba ndi kubadwanso mwatsopano (chimene chimachitika pa nthawi imodzi ndi chilungamitso). Ichi chimatchedwa chiyeretso choyamba, chimapirira kudzera mu chiyerenso chathunthu ndi ntchito ya nthawi zonse ya Mzimu Woyera pamene Mzimu akulungamitsa okhulupirira. Chimamalidzira mu ulemelero pa nthawi imene tamaliza kuumbidwa mu chifanizo cha Mwana wa Mulungu.

Timakhulupirira kuti pakutha pakubadwa kwa tsopano pali ntchito ya Mulungu imene okhulupirira amamasulidwa ku tchimo lobadwa nalo, amabweretsedwa ku mulingo wa kudzipereka kwathunthu kwa Mulungu, ndi kumvera chimene chiri chikondi cha ngwiro. Ichi chimatchedwa chiyeretso chathunthu.

Chiyeretso chathunthu chimakwaniritsidwa kupyolera mu ubatizo wa Mzimu Woyera, chimene chimatchedwanso kudzadzidwa ndi Mzimu Woyera, ndipo izi zimachitika pa nthawi imodzi kuyeretsedwa kwa mtima kuchokera tchimo ndi kukhazikika kwa Mzimu Woyera, kupereka mphamvu kwa okhulupirira ndi moyo wautumiki.

Chiyeretso chathunthu ndichotheka chifukwa cha mwazi wa Yesu, ndipo chimalandiridwa mwachisomo kupyolera m’chikhulupiriro, potsatira kuzipereka kwathtunthu; ndipo pantchito imeneyi chisomo cha Mzimu Woyera achitira umboni.

Ntchito ya chisomo imeneyi ikudziwika ndi maina ambiri amene akuimilira magawo osiyanasiyana monga: Chikhristu Changwiro, Chikondi Changwiro, kuyera kwa mtima, Ubatizo wa Mzimu Woyera, Chidzalo cha Mzimu Woyera, chidzalo cha Mdalitso ndi Chiyero Cha Chikhristu.

Timakhulupirira kuti pali kusiyana kwakukulu pakati pa mtima woyera ndi kukula m’chikhristu kapena kunkhwima mu chikhristu. Kuyera mtima kumachitka nthawi imene munthuyo wayeretsedwa kwathunthu; kukula mu chikhristu kumachitika monga zotsatira za kukula m’chisomo.

Timakhulupirira kuti munthu amene wayeretsedwa kwathunthu ali ndi chikhumbokhumbo cha kukula mu chisomo cha Mulungu monga ophunzira wa Yesu. Kukula kumeneko sikumachitika pakokha, koma kuyenera kusamaliridwa kudzera mukudzisunga m'moyo wa uzimu, kuti tikakhale monga Yesu m'chikhalidwe ndi mu umunthu. Iwo amene salimbikira kukula pa moyo wawo wa uzimu adzawononga umboni ndi chisomo cha Mulungu mu miyoyo kapenanso kutayika kumene.

Pakutenga nawo mbali mu ntchito za chisomo, makamaka chiyanjano, kudzisunga mmoyo wa uzimu, ndi masakalamenti a mpingo, okhulupirira amakula m'chisomo ndi chikondi chamngwiro pa Mulungu ndi pa anthu.

[Yeremia 31:31-34; Ezekieli 36:25-27; Malaki 3:2-3; Mateyu 3:11-12; Luka 3:16-17; Yohane 7:37-39; 14:15-23; 17:6-20; Machitidwe 1:5; 2:1-4; 15:8-9; Aroma 6:11-13, 19; 8:1-4; 12:1-2; 2 Akorinto 6:14-7:1; Agalatiya 2:20; 5:16-25; Aefeso 3:14-21; 5:17-18, 25:27; Afilipi 3:10-15; Akolose 3:1-17; 1 Atesalonika 5:23-24: Ahebri 4:9-11; 10:10-17; 12:1-2; 13:12; 1 Yohane 1:7, 9]

[“chikondi changwiro” Deutoronomo 30:6; Mateyu 5:43-48; 22:37-40; Aroma 12:9-21; 13:8-10; 1 Akorinto 13; Afilipi 3:10-15 Ahebri 6:1; 1 Yohane 4:17-18; [“Kuyera kwa mtima”: Mateyu 5:8; Machitidwe 15:8-9; 1 Petro 1:22; 1 Yohane 3:3; “Ubatizo wa Mzimu Woyera “: Yeremia 31:31-34; Ezekieli 36:25-27; Malaki 3:2-3; Mateyu 3:11-12; Luka 3:16-17; Machitidwe 1:5; 2:1-4; 15:8-9; “Chidzalo cha mdalitso”: Aroma 15:29; “Chiyero cha chikhristu”: Mateyu 5:1-7,29; Yohane 15:1-11; Aroma 12:1-15:3; 2 Akorinto 7:1; Aefeso  4:17-5:20; Afilipi 1:9-11; 3:12-15; Akolose 2:20-3:17; 1 Atesalonika 3:13; 4:7-8; 5:23; 2 Timoteo 2:19-22; Ahebri 10:19-25; 12:14; 13:20-21; 1 Petro 1:15-16; 2 Petro 1:1-11; 3:18; Yuda mavesi 20-21]

Mpingo

(The Church)

Timakhulupirira mu Mpingo, mbumba yomwe imavomereza Yesu Khristu kukhaka Mbuye wawo, Anthu amupangano la Mulungu amene akakhala atsopano mwa Khristu, thupi la Khristu lomwe linaitanidwa ndi Mzimu Woyera kudzera m'mawu.

Mulungu amaitana Mpingo kuti uonetse moyo wake mu umodzi ndi m’chiyanjano cha Mzimu; m’kupembeza kupyolera mu m’kulalikira kwa mawu, m’kusatira masakalamenti, ndi muutumiki mu dzina lake; pomvera Khristu, ndi kuzindikiritsana cholinga chake.

Utumiki wa mpingo m’dziko ndiwo kupitiriza ntchito ya Chiombolo ya Khristu mwa mphamvu ya Mzimu Woyera. Mpingo umakwaniritsa utumiki wake pakusula ophunzira kupyolera mukufalitsa Uthenga wa Bwino, m’maphunziro, m’ntchito za chifundo, m’ntchito za chilungamo, ndi kuchititra umboni za Ufumu wa Mulungu.

Mpingo ndi okhazikika m'madela ndi pa dziko lonse lapansi, ndipo umapatulira padera iwo oitanidwa ndi Mulungu ku mautumiki okhazikika. Mulungu amaitana Mpingo kukhala pansi pa ulamuliro Wake pamene ukuyembekezera kubweranso kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.

[Exodus 19:3; Yeremia 31:33; Mateyu 8:11; 10:7; 16:13-19, 24; 18:15-20; 28:19-20; Yohane 17:14-26; 20:21-23; Machitidwe 1:7-8;2:32-47; 6:1-2; 13:1; 14:23; Aroma 2:28-29; 4:16; 10:9-15; 11:13-32; 12:1-8; 15:1-3; 1 Akorinto 3:5-9; 7:17; 11:1, 17-33; 12:3; 12:31; 14:26-40; 2 Akorinto 5:11 -6:1; Agalatia 5:6 13-14; 6:1-5; 15; Aefeso 4:1-17; 5:25-27; Afilipi 2:1-16; 1 Atesalonika 4:1-12; 1 Timoteo 4:13; Ahebri 10:19-25; 1 Yohane4:17; Yuda vesi 24; chivumbulutso 5:9-10]

Ubatizo

(Baptism)

Timakhulupirira kuti ubatizo wa chikhristu, ndi sakaramenti lolamulilidwa ndi Ambuye wathu, umaonetsera kuti munthu wabvomereza phindu la chiombolo cha Yesu Khristu, uyenera kuperekedwa kwa okhulupirira ndipo umafotokoza za chikhulupiriro chawo mwa Yesu Khristu monga Mpulumutsi wao, ndipo cholinga chake chenicheni ndi kukhala omvera m’chiyero nd mu ungwiro.

Ubatizo ndi chizindikiro cha pangano la tsopano, kotero, Ana ang'ono akhoza kubatizidwa, potsatira phempo makolo awo kapena amene akuwasunga ngati angalonjeze kuwalera ndi kuwakuza iwo mu njira ya chikhristu.

Ubatizo ukhoza kuchitika pakumuwaza munthu madzi, pakumuthira munthu madzi, kapena kumumiza munthu mu madzi, zonsezi zichitika mwa kusankha kwake kwa munthu amene ali kubatizidwayo.

[Mateyu 3:1-7; 28:16-20; Machitidwe 2:37-41; 8:35-39; 10:44-48; 16:29-34; 19:1-16; Aroma 6:3-4; Agalatia 3:26-28; Akolose 2:12; 1 Petro 3:18-22]

Mgonero wa Ambuye

(The Lord’s Supper)

Timakhulupirira kuti chikumbukiro ndi chiyanjano cha Mgonero wa Ambuye chimene chinakhazikitsidwa ndi Ambuye wathu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu ndi sakaramenti limene lili ndichiyambi chake m'Chipangano Chatsopano, limalalikira za imfa Yake, imene ili nsembe kupyolera mu imfa imeneyi okhulupirira ali ndi moyo ndi chipulumutso ndiposo lonjezo la madalitso onse a uzimu mwa Khristu. Ndipo ndi la kwa iwo wokhawo amene okonzekera kulemekeza moyamika kufunika kwake, ndipo kupyolera mu Mgonero umenewu iwo amaonetsa imfa ya Ambuye mpaka Iye atabweranso. Tsono amene ayenera kuyandikira ku Gome la Ambuye ndi iwo okha amene akhulupirira mwa Khristu ndi iwo okhala ndi chikondi kwa anthu Oyera Mtima.

[Eksodo 12:1-14; Mateyu 26:26-29; Marko 14:22-25; Luka 22:17-20; Yohane 6:28-58; 1 Akorinto 10: 14-21; 11: 23-32]

Machiritso Ochokera Kwa Mulungu

(Divine Healing)

Timakhulupirira m’chiphunzitso cha M'buku Lopatulika chofotokoza za machiritso ochokera kwa Mulungu ndipo timalimbikitsa akhristu athu kupemphera pemphero la chikhulupiriro kuti odwala alandire machiritso. Timakhulupiriranso kuti Mulungu amachiritsa kudzera m'njira za chipatala.

[2 Mafumu 5:1-19; Salimo 103:1-5; Mateyu 4:23-24; 9:18-35; Yohane 4:46-54; Machitidwe 5:12-26; 9:32-42; 14:8-15; 1 Akorinto 12:4-11; 2 Akorinto 12:7-10; Yakobo 5:13-16]

Kubwernso Kachiwiri Kwa Khristu

(Second Coming of Christ)

Timakhulupirira kuti Ambuye Yesu Khristu adzabweranso kachiwiri; ndikuti ife amene tili amoyo pa kubweranso kwake sitidzagolera akugona mwa Khristu Yesu; koma kuti, ngati tikhala mwa Iye, tidzakwatulidwa pamodzi ndi Oyera mtima kukumana ndi Ambuye mlengalenga, kuchokera pamenepo tidzakhala ndi Ambuye ku nthawi zonse.

[Mateyu 25:31-46; Yohane 14:1-3; Machitdwe 1:9-11; Afilipi 2:20-21; 1 Atesalonika 4:13-18, Tito 2:11-14; Ahebri 9:26-28; 2 Petro 3:3-15; Chivumbulutso 1:7-8; 22:7-20]

Chiukitso, Chiweruzo, Ndikokhala

(Ressurection, Judgement, and Destiny)

Timakhulupiria mu chiukitso cha akufa, uku ndiko kunena kuti, matupi a anthu olungama ndi osalungama adzaukitsidwa ndi kukhalanso ndi moyo ndikulumikizidwa ku mizimu yawo – “… amene adachita bwino adzakhala moyo osatha, koma amene adachita zoipa adzalangidwa kosatha.”

Timakhulupirira kuti pali chiweruzo chimene chilinkudza pamene munthu aliyense adzaimilira pamaso pa Mulungu kukaweruzidwa monga mwa ntchito zake m’moyo uno.

Timakhulupirira kuti iwo amene anapulutsidwa pakukhupirira Yesu ndikumvera pomusatira Iye ali ndi lonjezano la ulemelero wa moyo osatha. Iwo okana kulapa adzazunzika kosatha ku gahena ku nthawi zosantha.

[Genesis 18:25; 1 Samueli 2:10; Salimo 50:6; Yesaya 26:19; Danieli 12:2-3; Mateyu 25:31-46; Marko 9:43-48; Luka 16:19-31; 20:27-38; Yohane 3:16-18; 5:25-29; 11:21-27; Machitidwe 17:30-31; Aroma 2:1-16; 14:7-12; 1 Akorinto 15:12-58; 2 Akorinto 5:10; 2 Atesalonika 1:5-10; chivumbulutso 20:11-15; 22:1-15]

Tabs

WHDL ID: 
WHDL-00001095
Tablet Validation: 
Suitable